Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Kiwano – Cucumis metuliferus

Zipatso za Kiwano zazitali 10–15 cm zimaoneka ngati malalanje. Zili mugulu la minkhaka. Zipatso zake zili ndi tinyanga tating’onoting’ono pa makoko ake ndipo zimamupangitsa munthu kuganizira za chida cha nkhondo. Mnofu wa chipatso ndiwobiliwira ndipo nthawi zambiri umakhala ndi njere zoyera zambiri zazitali 5–10mm.

Zipatsozi zimachokera ku Izirayeli ndiku Chigawo chapakati cha Amerika. Timadya mnofu wobiliwirawu limodzi ndi njere. Kiwano amakoma ngati nkhaka, marrow ndi nthochi. Tikatha kudya kiwano, tikhonza kugwiritsa ntchito chikombe chakunja kwake ngati mbale zokongola; pomwe njere zake tingadzale. Ndimbewu yokula msanga imene imaoneka ngati ma marrow a misinde ndi zoyanga zazitali. Masamba ake amampangitsa munthu kuganizira za nkhaka poti naonso ali ndi titsitsi tating’onoting’ono tobaya.

Pollination ya maluwa atali 3 mm ndi chimodzimodzi monga ichitira mbewu ya nkhaka. Tizindikire kuti chipatso chikhonza kuola chikafika pogundana ndi dothi. Kiwano amamera bwino ndi temperature yozungulira 25 ºC, choncho temperature ya m’mabokosi wamba imasungidwa chimodzimodzi ngati momwe apangira ndi nkhaka komanso mavwembe/mameloni. Kiwano imapilira malo osazizira kwambiri. Ngati mukukhala kumalo kumene kumazizira kapena kumene madzi amaundana chifukwa chakuzizira, ndikoyenera kudzala kiwano panja madzi owundana akatha.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Mpoza (Annona cherimola) Nkhani yotsatira: Kodi ndikugwetsa bwanji nankafumbwe wa nyemba? »»»

Lachitatu 2. November 2011 20:56 | purintani | Zomera za chilendo

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi