Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

NOVODOR FC wolimbana ndi nankafumbwe wa mbatata

Sindikuganiza kuti ndikuyenera kulongosola za nankafumbwe owononga mbewu ya mbatata (Leptinotarsa decemlineata) popeza aliyense akudziwa za chirombo choipachi chimene chimaononga kwambiri mbatata ndipo sikotheka kuzigonjetsa popanda kugwiritsa ntchito mankhwala. Panopa, palibe akudziwa mankhwala enieni amene angagwiritsidwe ntchito pophera nankafumbwe owononga mbewuyu.

Kodi amachokera kuti?

Nankafumbweyu anachokera kumpoto kwa Amerika mpaka Europe. Kumeneko nankafumbwe samapezeka chisawawa kudera la Cordillera kumene amadya masamba a mbatata zamutchire. Pamene anthu anayamba kulima mtundu wa mbewu uwu (dzina lachi botanic: Solanum tuberosum) malo ambiri aku Amerika, nankafumbweyu anadzichotsa ku mbatata zamutchire kupita ku mbatata zolimidwa. Tithokoze mbatata, nankafumbweyu anafalikira padziko lonse lapansi.

NOVODOR FC – Mankhwala enieni olimbana ndi Nankafumbwe?

Novodor FC ali ndi 2% ya zakudya zomanga thupi kuchokera ku tizirombo ta Bacillus thuringiensis ssp. tenebroinis. Mpikisano wa tizirombowu umawononga ndi mphutsi zomwe zochokera gulu la Galerucinae (umawononga mitengo monga ngati mtengo waphulusa) ndi nankafumbwe owononga mbatata.

Izi zimayambitsa matenda a mphutsi a mtundu umene tatchulawu. Mukadya Masamba amene athiridwa mankwala, mphutsi zimasiya kudya ndipo pakatha masiku 2–5 zimafa chifukwa chamankhwala. Kwamphutsi zina izi sipoizoni, sizimayambitsa vuto lina lili lonse, osati kwa masamba kapena kwa dothi lake. Mphutsi zimaonongedwa ndi izi pamene zikadali zazing’ono osati zitakula. Zigwiritsidwe ntchito pa mphutsi zazing’ono.

Kuti muwone kufinikira kwake kwa izi, ndikofunikira kuti mphutsi zizidya mkati – kotero ndikofunikiranso kuthira pamwamba ndi pansi pamasamba bwino lomwe ndi mankhwala. Ndibwino kuthira mankhwalawa pamene kulibe mphepo ndipo kwa temperature yoposa 15 °C. ngati kwagwa mvula mkati mwa maola 12 mutathira mankhwala, chisamaliro chibwerenzedwe.

Mankhwalawa amagulitsidwa m’mapaki ang’onoang’ono, mumabotolo ang’onoang’ono a galasi a 100 ml ndipo mtengo wake ndi kuzungulira 3€ basi.

Mtundu wina wa tiziromboti umapha mphutsi za gulugufe wa kabichi (Pieris brassicae) ndi gulugufe wa Codling (Cydia pomonella) (substance Biobit FC) ndi udzudzu.

Pomaliza nkhani yabwino: Chipatso (babu) chikhonza kudyedwa pompopompo chikangotuluka

««« Nkhani ya m’mbuyo: Kudzala mababu a maluwa ndi mmera

Lolemba 12. November 2012 12:21 | purintani | Tizilombo towononga mbewu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi