Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Kudzala mababu a maluwa ndi mmera

Chotsani mababu a maluwa ndi mmera amene mwalandira pa positi muphukusi, ndipo zisiyeni zikhale mumthunzi kwa masiku awiri kapena atatu. Chothekera chachiwiri ndikuzidzala nthawi yomweyo ndikuzisunga mumthunzi kwa masiku ochepa kuti zisafote ndi dzuwa.

Kudzala mmera

Pangani mphako yaing’ono kuti mudzalemo mmera. Chotsani mmera mumphika (kuchokera mthumba la pulasitiki mmene mmera aulongedza mosiyana), tembenuzani mizu motsitsa pansi ndikuibalalitsa mofanana musanaike mbewu yonse mumphako.

Thirani madzi mumphako ndipo dothi likamwa madzi onse, thirani madzi ena ambiri. Samalani mbewu zina zonse chimodzimodzi monga mwachitira. Mukathana ndi mbewu zonse, zithilireninso.

Masiku angapo oyambilira mukadzala, mukhonza kuzithilira potsatira ndondomeko yake yokha ndikuzisamalira kuti zisawauke ndi dzuka. Mbewu zidzamera mizu pakapita mulungu umodzi mpaka itatu kenako mukhonza kumazisamalira mwadongosolo chimodzimodzi ndi momwe mumasamalira mbewu zina zonse mmunda mwanu.

Kudzala mababu a maluwa ndi mmera

Choyambilira kumbani dothi limasuke pamene mukufuna kudzala mababu ndi matuber (tigwiritsa ntchito liwu loti mababu muzofotokoza zathu zonse). Chotsani mababu mupepala nthawi imene mukufuna kudzala.kumbani dzenje lalitali bwino (onani tebo) ndipo ikani babu mudzenje, kumtunda kuyang’ane mmwamba. Mababu ena samapulumuka mukawadzala pamwamba pake pataloza pansi – samalani bwino lomwe powadzala moyenera!

Ngati mwadzala tulips pakati panyengo yotentha / yachilimwe (mwina simungamusunge paliponse kapena mukupita ku tchuthi) simukuyenera kumupatsa madzi. Mababu adzapuma ndipo adzayambanso kukula mvula yoyambilira ya nyengo ya autumn ikadzagwa.

Mababu ocheperako ovuta kukula, akuyenera kudzalidwa padzenje losaya kwambiri. Kuti mupeze mulingo wakuya kwa dzenje lomwe mukufuna kudzalapo mbewu, ndibwino kuyeza matalikidwe a pakati pa mmwamba mwa babu kufikira pa nthaka!

Timachotsa mababu m’dothi pamene chapamwamba (pamwamba pa nthaka) chafota (ili ndi lamulo la mababu a maluwa onse kupatula Gladiolus) – ichi chikhonza kukhala chifukwa chofulumilira monga mwezi wa May ku Ulaya (nthawi yotentha ndi youma). Mitundu yambiri ikhonza, itafukulidwa pansi, kusungidwa (bolani isungidwe youma) mpaka autumn (makamaka anyezi, adyo, saffron ndi tulips).

Mitundu yotsala monga mwachitsanzo lily, grape hyacinth (Muscari), Ornithogalum, ndi solomon's seal (Polygonatum) sizingasungidwe chonchi, pakuti zikhonza kufa. Mitundu imene siyingasungidwe (malo owuma) ndibwino kuyidzala kuchoka pamalo ena mmunda mwanu kupita malo ena (ikhonza kukhala ndi moyo mulungu umodzi, koma siyoyenera kuyisunga panja kwa nthawi yaitali kuposa apa).

Species planting period kuya kwa mbewu m‘ma sentimita
Mitundu yaing’ono yokhala ndi mulingo wa mababu ya 2cm monga the Allium carinatum, flavum, molly, oleraceum, scorodoprasum 7.-10. 5–8
Mitundu yaikulu yokhala ndi mulingo wa babu ya 10cm monga the Allium giganteum, karataviense, nigrum 7.-10. 10–15
Colchicum – mitundu imene imasasatuka nyengo ya autumn 8. 15
Crocus – mitundu imene imasasatuka nyengo ya mvula (Crocus chrysanthus, Crocus vernus) 10. 9
Crocus – mitundu imene imasasatuka nyengo ya autumn (Crocus sativius) (7.-)8. 9
Gladiolus (garden hybrids) 4.-5. 10 (kuchepa kuposa 5)
Gladiolus (mitundu wa chilengedwe yaku South Africa) 9. 5–8
Lilium candidum –lily woyera kapena or lily wa Madonna 8. 3
Lilium –ma hybrid a mmunda 9.(-10.) 5–15 kutengera ndi mtundu wake
Muscari – grape hyacinth 7.-10. 8–10
Narcissus – narcis 8. 10
Ornithogalum umbellatum – Nyenyezi-ya-Bethlehem, Lily wa udzu 7.-10. 10
Polygonatum – salomons seal 8.10., 2.-3. 10
Tulips okhala ndi mababu ang’onoang’ono monga Tulipa chrysantha, tarda, saxatillis, turkestanica, urumiensis 10. 10
Tulip okhala ndi mababu akuluakulu – Tulipa greigii, Tulipa fosteriana, Tulipa kaufmanniana ndi garden hybrids 10. 12–14

Lily Kuchuluka kudzera m‘masikelo

chithunzi

Kuchulukana kwa lily ndi masikelo

Njira yophweketsetsa yochulukitsira lily pogwiritsa ntchito ma sikelo (ma leya a babu)

Dzalani masikelo mmilu ya dothi yakuya 1–2 cm (=kutalika kwa dothi lotchingira masikelo) ndipo asungeni m‘matemperature a 25–30 ºC masana ndi 22 ºC usiku (temperature ya usiku ikhonza kukhala yochepera, yofunikira kwambiri ndi temperature ya masana) mwachitsanzo bodi ya makapu, nkhokwe kapena sill ya window mkati mwa nyumba yanu. Sungani dothi liri louma. Pakutero mababu atsopano adzaphuka pansi pa masikelo. Mu mwezi umodzi mpaka miyezi itatu, mababu awari kapena atatu a 1cm akhonza kuyamba pa imodzi mwa masikelowa! Ngati mwasenda masikelo ndikuwadzala mwezi wa July, mukhonza kuchotsa mababu atsopanowa mudothi mu Sepitembala ndikuwadzala pansi papatali 2cm m’munda. Dzalani babu yatsopano iliyonse payokha, ndikuisiya pafupifupi 4cm pakati pa babu iliyonse – pakutha pa zaka 4–6 mudzakhala ndi mababu a maluwa okongola kwambiri!

Kudzala njere za mababu a maluwa

Mababu a maluwa ena akhonza kuchulukitsidwa mwachangu ndi mothekera pogwiritsa ntchito njere. Ku Ulaya nthawi yabwino yodzalira njere 0.5–1cm kulowa pansi ndi miyezi ya March mpaka April. Osazidzala mchaka choyamba, koma zisiyeni pomwe zili mmalo omwe zafikira. Mitundu ina idzakhala itasasatuka kale mnyengo yotsatira. Komabe yambiri mwa mitundu iyi imayamba kusasuka pakati pa zaka ziwiri mpaka zisanu mukadzala. Mitundu yaing’ono imasasuka msanga kusiyana ndi mitundu yokulirapo ya ma babu okulirapo.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Kulima bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) Nkhani yotsatira: NOVODOR FC wolimbana ndi nankafumbwe wa mbatata »»»

Loweruka 26. November 2011 14:03 | purintani | Malangizo a kalimidwe ka mbewu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi