Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Palmu Parajubaea torallyi (Palma Chico, coconut wam’phiri la Bolivian)

Parajubaea torallyi ndi palmu wamphamvu wokongola ochokera ku m’mwera kwa America. Koma, siumalimidwa kawirikawiri ndi osamalira zomera a kunja kwa dziko la chilengedwe chake, Bolivia, chifukwa chakukula kwa masamba ake (kutanthauza kuti mtengo wake wotumizira ndiwokwera).

Ndiwobadwira ku Bolivian, umamera kowuma ndi kwa fumbi, ku zigwa za inter-Andean pa mamitala 2700–3400 pamwamba pa Nyanja. Kotero kuti, mtundu wa palmu umenewu ndiwokwera kwambiri kulikonse padziko lonse. Mpweya wake sukonda kukwera pamwamba pa 20°C ndipo mphepo ya usiku yozizira kwambiri siyimasowa m’menemu. Mpweya umakonda kutsika mpaka –7°C mu miyezi ya dzinja (July ndi August) ndipo mvula yapachaka ndi mamilimitala 550 basi.

Imalora kokokoloka madzi, kotentha, kozizira, kwa mphepo yozizira, ndi nyengo zina, ndipo kuwoneka bwino kwake, kumayambitsa ena kunena kuti palmu ameneyu siwongokongola kokha ayi komanso akhonza kukhala m’modzi mwa mapalmu osilirika a mpweya wotentherako ndi madera wotentherako. Kumadera komwe kuli mphepo yozizira kwambiri palmu ameneyu amafuna chitetezo ku dzinja kapena kusunga malo osadutsa mphepo yozizira kwambiri. Zinanenedwa kuti ku Europe kumazizira mpaka –3°C. mpweya ochepetsetsa omwe palmu ameneyu anakwanitsa atalimidwa anali –8°C. Zomera zimenezi zinayoyoka masamba onse, koma kukulabe ndipo munyengo yamvula, masamba atsopano anawoneka!

Ku Bolivia, palmu ameneyu amatalika mpaka mamitala 14 ndi thunthu la mtengo lamasentimitala 25–35 mu dayamita. Ma palmu amene ali ndi zaka 100 kapena kuchulukira, amatalika mpaka mamitala 30 m ndi thunthu lamasentimita 50 mu dayamita. Tsonga labwino limakhala ndi masamba okwanira 20 ndipo ena mpaka kutalika mamitala asanu (5)! Zomera zakunja kwa Bolivia zimakhala zocheperako.

Muli zowoneka ziwiri muchilengedwe zimene zili zosiyana makamaka mu muyeso wa zipatso zake ndipo posachedwapa zinatchedwa ngati magulu awiri osiyana, la zipatso zazing’onozing’ono P. torallyi var. microcarpa ndi la zipatso zazikuluzikulu P. torallyi var. torallyi. Ngakhale zisali zosiyana kwenikweni mumawonekedwe ake, var. microcarpa sizimafika penipeni pa m’bale wake wa zipatso zazikulu, Koma kutengera ndi kukwanira kwake ndi mphamvu zake, zimafanana. Ntchito zake za njere sizichita bwino pakusadalira kumera. Ngakhale kumera nthawi zina kolakwika, njereyo imamasulabe mosavuta ngati yabzyalidwa moyenelera, monga pa mizere, itakwiliridwa theka la mkati mwa mzere, ndipo liri pa chinyezi. Mosamalira, ndi nyengo yazizilirako mpaka yotentha pang’ono ndi malo a dzuwa, njere zimafulumira kukula, kutalika, kukhala ndi thunthu zamphamvu za palmu ndi Tsonga zikuluzikulu, masamba okhala ngati chikopa. Kulora kukhala mu nyengo youma kwake, kutentha, kuzizira, mphepo yozizira kwambiri, ndi mitundu ina ya nyengo, ndikukwanitsa kwake kuwoneka kukongola, zimapangitsa ena kunene kuti palmu wabwinoyu siwongokhala ndi mphamvu zokhalira chomera chokongoletsera, koma kuti ikhonzanso kukhala imodzi mwa palmu wosilirika ku Madera kotentherako komanso kumadera kotentha.

Parajubaea torallyi ndi maluwa otchuka ndipo amakonda kudzalidwa kumapaki ndi mphepete mwa msewu. Ku Ecuado ndi kum’mwera kwa Columbia, Parajubaea cocoides amakonda kulimidwa komwe kutalika kwake ndi mamitala 2500 mpaka 3000 – uwu ndi palmu okula pang’onopang’ono ndipo osagwirizana kwenikweni ndi mphepo yozizira kwambiri. Monga zifananira ndi Parajubaea torallyi ndipo chilengedwe chake sichidziwika, zinaloredwa kuti ndizolimidwa zaku Parajubaea torallyi

Wochepetsetsa wa motundu wa palmu ameneyu ndi Parajubaea sunkha womwe unadziwidwa muchaka cha 1996. Umatalika mamitala 8 okha ndipo umapezeka kuzigwa za Andean kuchigawo cha Vallegrande, m’boma la Santa Cruz ku Bolivia komwe kutalika kwake ndi mamitala 1700–2200. Zakhala zikuzindikirika molakwika ngati Parajubaea torallyi mpakana kafukufuku wapompano anapangidwa ndipo inatchulidwanso kukhala Parajubaea sunkha.

Mapalmu a gulu la Parajubaea ndiwosavuta kulima. Njira yabwino yolimira ndi yogwiritsa ntchito njere. Komabe, mukuyenera kudekha pamene njere zikumera pang’onopang’ono ndipo mosafanana mutchire, ndiponso zimatenga chaka chimodzi ndi theka kuti zitero. Njere zina zimayamba kumera mkatikati mwa mwezi, koma zina zimakhala chaka chonse mwinanso zaka ziwiri kuti ziyambe kumera. Monga uli mtundu wa palmu womera kudera lotentha, ndibwino kumusunga kumalo nyengo yotsika, poti ku malo a nyengo yokwera (kusiyana ndi mitundu ina ya palmu) yomwe ingakhale ndi ndondomeko yake yosiyana ndi kameredwe kameneka. Nyengo yokwera itanthauza nyengo yowuma, yomwe siyabwino pa zomera.

Musanabzyale, njere siyikidwe m’madzi ndi mpweya wa pafupifupi 20°C kwa masiku 5 mpaka 7. Njere za mtundu wa njere zazikulu siyikidwe m’madzi kwa milungu iwiri. Madziwo azisinthidwa tsiku liri lonse. Njere zikhonzanso kuperekedwa popereka mwayi kuti zimere.

Kuviyika kwa njere m’madzi zidzatsindika nthawi yeniyeni zisanamere ndipo zimayambira nthawi ya mvula, yomwe ili nthawi yabwino kwambiri kumera. Nthawi yoyembekezera kumera imateteza njere kuti isayambe kumasula nthawi ya dzuwa ku Bolivia (nyengo ya dzinja mu June mpaka October)

Mukatha kunyika, njere zibzyalidwe mumphika kapena pepala la pulasitiki – samalani kuti theka lokha likwiliridwe ndi dothi ndipo sungani mu mpweya wa 10 mpaka 20°C.

Zopatsa chikoka pa zomera zomera bwino ndi kusiyana pakati pa tsiku (m’mwamba) ndi usiku (m’musi) mpweya. Mukangobzyala njere, zisathiliridwe kwambiri popeza madzi ambiri akhonza kuwononga zomera zing’onozing’ono. Kusiyana kwakukulu pakati pa kulima Parajubaea ndi mitundu yina ya palmu ndi mpweya wotsika umafuna chimodzimodzi madzi wochepa.

Mukatha kubzyala, njere zizipangidwa tcheki milungu itatu kapena inayi ili yonse ndipo njere zomasula kale zisungidwe m’miphika, wakewake. Olima palmu ena anapereka malangizo awa okhudzana ndi njere zomwe sizinamasule pakutha pa miyezi inayi:

Lekani kuthilira njere ndipo lekani dothi liwume kwa miyezi yochepa. Chotsani njere m’dothi, ziyikeninso m’madzi kwa mulungu umodzi kenaka zibzyaleninso.

Njere zimenezi ziyambe kumasula mkatikati mwa theka la chaka chotsatiracho. Ngati njere zina sizinamasulebe, bwerenzani njira yomwe ija ndipo njere zonse zotsala zidzamasula pakutha pa nyengo ya mvula yotsatirayo.

Muyeso womelera wa njere za Parajubaea ndi pafupifupi 100%, chongofunika ndikudekha mokwanira, ndipo lorani nyengo yowuma kwa njere zaulesizo!

Mukangokhala ndi palmu wam’ng’ono, ndi wamphamvu, koma kumbukirani kumuthilira kwambiri. Palmu wam’ng’ono amafuna malo a mpweya wapakatikati potentha ndipozizira (mu chilengedwe chawo amakula pansi pa mthunzi wa mitengo yapamu yayikuluyikulu), komabe yokulirapoyo imafuna kukhala pa dzuwa.

Gulu la Parajubaea ndi limodzi mwa mitengo ya palmu yaku m’mwera kwa dziko la America lomwe ndilotetezedwa. Chifukwa chachikulu chakuwonongekera kwa chilengedwe, kufalitsa kwa malo olimapo, kudula mitengo ndi kudyetsa ziweto. Ma palmu amenewa amachitika ku dera laling’ono kwambiri, zomwe zikupangitsa chisamaliro kukhala chotsimikizika ndipo zikhonza kufa. Chifukwa chakukula kwa njere za mbewu zimenezi, kufalikira kwake ndikwamalire. Nyama yofunikira kwambiri kuthandiza ma palmuwa kufalikilira ku madera atsopano ndi Insa (Tremarctos ornatus), komabe nyama zimenezi zimaopa zochitika za anthu.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Indian Lotus Nelumbo nucifera zomera za m’madzi Nkhani yotsatira: Pinus kesiya - Khasi Pine, Paini wa Khasi »»»

Lachiwiri 19. May 2009 18:16 | purintani | Mapalmu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi