Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Pongamia pinnata

chithunzi

Pongamia pinnata

Chinsense Pongamia pinnata (maina ena: Honge Tree, Pongam Tree, Panigrahi) ndi mtengo umene umapululuka masamba nyengo yozizira, pakati pa mamitala 15–25 kutalika, umene uli m’gulu la Fabaceae. Uli ndi m’mwamba mwamukulu ndi maluwa ang’onoang’ono ambiri oyera, pinki kapena violet. Unabadwa ku India, koma unafalikira kulimidwa ku m’mwera chakuvuma kwa Asia.

Pongamia pinnata ndi mtengo olimba, osaopa kutentha ndi dzuwa. Tithokoze chifukwa cha mizu yake yayikulu, umaloranso pamene kuli chilala. Pachilengedwe chake, umamera padothi la mchenga kapena miyala, kuphatikizapo miyala ya laimu, koma nyengo yolima, ukhonza kumera bwinobwino pafupifupi m’dothi la mitundu yonse kuphatikizapo dothi la mchere.

Umakonda kulimidwa malo owuma ndipo umakonda kugwiritsidwa ntchito pokonza malo ngati chotchingira mphepo kapena ngati mthunzi. Makungwa ake amagwiritsidwa ntchito kupangira twaini kapena zingwe, ndipo ulimbo wake wakuda wakhala ukugwiritsidwa ntchito m’mbuyomu kuchiritsira zilonda zoyamba chifukwa cha nsomba za poizoni.

Mizu yake yooneka motupa ikhonza kugwiritsidwa ntchito ngati manyowa a nthaka imene ilibe zakudya zokwanira. Ngakhale mbewu yonse ili poizoni, madzi ochokera ku mbewuyi, pamodzi ndi mafuta ake, amapha tizilombo mthupi. Mafuta a m’mbewuyi amagwiritsidwa ntchito ngati mafuta a nyali, kupangira sopo, kufewetsera makina kuti azigwira ntchito bwino, ndi kupangira bio-dizilo.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Kalimidwe ka Four Leaf Clover (Marsilea quadrifolia) Nkhani yotsatira: Kulima bowa wa mzikuni (Pleurotus ostreatus) »»»

Lachinayi 24. November 2011 19:59 | purintani | Zomera za chilendo

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi