Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Mango aku Indonesia

Pachilumba cha Borneo ku Indonesia pali mitundu ya mango yokwana makumi atatu ndi mphambu zinayi (Mangifera) yomwe ndi yachilengedwe. Mitundu yambiri ili pachiwopsyezo cha kusapezekanso chifukwa cha kugwetsedwa kwa mitengo. Ina mwa mitundu ya mangowa, monga mango a Kalimantan (Mangifera casturi) atha kale mutchire, sakupezekamo.

Mitengo ina ya mango yochokera ku Borneo ndi monga Mangifera griffithi (yodziwika ndi maina awa: asem raba, ndi romian), Mangifera pajang (asem payang), Mangifera quadrifida (asem kipang) ndi Mangifera torquenda (asem putaran).

Mango onunkhira (Mangifera odorata) ndi mtundu wa mango wotchuka omwe umalimidwa kawirikawiri kum’mwera chaku mvuma kwa dziko la Asia. Ndi mtundu waukulu pakati pa mitundu yomwe imakonda kulimidwa (Mangifera indica) ndi Horse Mango (Mangifera foetida). Umadziwika ndi maina a mderalo monga: kuweni, kuwini (m’chilankhulo chachi Indonesia); kweni, asam membacang, macang, lekup (m’chilankhulo chachi Malay); kuwini, ambacang, embacang, lakuik (m’chilankhulo chachi Minangkabau); kuweni, kebembem (m’chilankhulo chachi Betawi); kaweni, kawini, bembem (m’chilankhulo chachi Sundan); kaweni, kuweni, kweni (m’chilankhulo chachi Javan); kabeni, beni, bine, pao kabine (m’chilankhulo chachi Madurese), kweni, weni (m’chilankhulo chachi Balinese); mangga kuini (ku mpoto kwa Sulawesi); ndi kuini, guin, koini, kowini, koine, guawe stinki, sitingki, hitingki (pazilumba za Maluku).

««« Nkhani ya m’mbuyo: Fodya wa Mtengo Nicotiana glauca – Chomera chokongoletsa pamalo perspective! Nkhani yotsatira: Mango a Kalimantan, Kasturi (Mangifera casturi) »»»

Lamulungu 20. November 2011 19:44 | purintani | Mapalmu

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi