Botanix – Buku la zomera

Botanix ya Chicheŵa

Fodya wa Mtengo Nicotiana glauca – Chomera chokongoletsa pamalo perspective!

chithunzi

Fodya wa Mtengo (Nicotiana glauca)

Khumbo la munthu ku chinthu chatsopano ndi chosachitikachitika lilibe malire. Alimi naonso amalota za chinthu chatsopano chimene angalime mmunda mwawo – chimene aliyense alibe. Msika wa mbewu nawonso umakhala ndi zinthu zatsopano za alimi – ndi cholinga choletsa njala imene alimi ofuna zinthu zabwino amakhala nayo. Kukhanzikitsidwa kwa malonda a mbewu zatsopano, kudzapangitsa kuti mitengo ya fodya izipezeka paliponse kwa alimi onse posachedwapa!

chithunzi

Fodya wa Mtengo (Nicotiana glauca)

M’zaka khumi zapitazo zosinthika kwambiri muzomera ndizochokera m‘gulu la nightshade (Solanaceae). Zodziwika bwino mwa zinthuzi ndi petunia, surfinia, ndi million bells (Calibrachoa). Chinsinsi chawo chagona pa kukula mwachangu, kutulutsa maluwa msanga (imatulutsa maluwa mkati mwa miyezi itatu ngati mwadzala njere zake, ndipo ngati mwadzala mitengo yodula, maluwa amatuluka nthawi yomweyo) ndi kusafuna zinthu zambiri kuti ikule bwino. Imafuna malo a dzuwa, koma imakulanso malo a mthunzi ndi ozizilira.

Ngakhale zili choncho, mbewu zochokera m’gulu la nightshade sizinatchuke. Mwachitsanzo taganizirani za mbatata ndi tomato amene nthawi ina yake analimidwa chifukwa cha kukongola kwake basi! Pamene mbiri inawanda kuti mbewu zimenezi zikhonza kudyedwa, munthu anali wodabwa kwambiri. Tsopano zikudyedwa kwambiri m‘maiko ambiri ndiponso zakudya za chikhalidwe chathu zikupereka danga kwa mbewu zimenezi!

chithunzi

Munkhani iyi tikuuzani za mbewu ya Fodya wa Mtengo (Nicotiana glauca) – yochokera ku mmwera kwa Amerika. Ndi mtengo wokula msanga. Umatulutsa maluwa pakatha miyezi iwiri yokha mukadzala, ndipo nthambi zake za mtengo waukulu zimakula 50–70cm mkatikati mwa mwezi woyamba.

Mwa dzina lake lachiLatini (glauca = grey), mtengo wokwanira bwinobwino umakhala ndi mtundu wa siliva. Kotero, sufunika kukhudzidwa chifukwa suchedwa kusintha mtundu wake wabwino wa siliva wa phulusa kupita ku mtundu wosaoneka bwino wobiliwira mowala. Masamba ake ndi a siliva wachi phulusa, amaonekedwe ozungulira ndi osongoka kumapeto. Kumapeto kwa nthambi kumakhala nthambi zazing’ono za maluwa 20–40 a chikasu akulu mmwamba ndi a ng’ono pansi. Maluwa ake ndi atali 3–3.5cm ndipo kuzungulira 0.5cm mulifupi. Pamayambiliro a nthawi yotulutsa maluwa pamakhala mtundu wobiliwira ndi wachikasu owala kumapeto. Maluwa akatuluka, amakhala achikasu chokuda . ubwino wa mbewu imeneyi ndiwakuti maluwa amakhala akukongoletsa ngakhale utatha kupanga maluwa. Kusiyanitsa ndi mwachitsanzo Petunia, maluwa ake amasunga maonekedwe ake ndikupitiliza kukhala kumitengo yake kwa nthawi yaitali.

Kulima mtunduwu ndikosavuta. Mukhonza kusunga mtengo wa fodya (Nicotiana glauca) mkati mwa nyumba kapena panja nthawi ya chilimwe. Mukhonza kuyichulutsa pogwiritsa ntchito njere zimene zimamera kwambiri ndi mwa mphamvu. Mbewu zidzayamba kututsa maluwa mkati mwa miyezi iwiri (choncho ngati mukufuna kuti zitulutse maluwa kuyambira mwezi wa May, mukuyenera kuzidzala m’mwezi wa Marichi).

Ngati mukukhala kumadera kumene madzi amaundana chifukwa chakuzizira kwambiri, mukuyenera kusunga fodya malo amene sapezana ndi madzi oundanawo. Monga ndi Pelargonium, mukhonza kusunga mbewu zimenezi malo ozizilirapo (koma owala) m‘nyengo ya dzinja. Nyengo ya dzinja ikatha, mukhonza kusadzula nthambi ndi theka ndikuzipatsa madzi ambiri. Mbewu iyi ikhonza kupanga mtengo mosavuta, umene mungasunge mnyumba mwanu. Koma simungaudzale pogwiritsa ntchito mitengo yodula poti imavuta kumera mizu (komabe ichi chisakhale chiphinjo poti kuudzala pogwiritsa ntchito njere, ndikosavuta).

Kukamba za zakudya za mbewuyi, mbewu ya fodya siilira zambiri. Kukhala ndi mbewu ya maluwa okongola, mukhonza kuyithila manyowa wamba ndi feteleza wa mchere pang’ono.

««« Nkhani ya m’mbuyo: Ulimi wa Welwitschia mirabilis Nkhani yotsatira: Mango aku Indonesia »»»

Loweruka 19. November 2011 19:31 | purintani | Zomera za chilendo

Mbiri ya KPR

Chizindikiro cha KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera ku Slovakia
KPR - Bungwe la anthu osamalira zomera la KPR ndi bungwe lapadziko lonse lapansi. Werengani zambiri...
Gawani zomwe mukudziwa za kubyala mbewu komanso kusamalira zomera. Lembani nkhani zokhudza kubzyala ndi kusamalira mbewu komanso zomera, ndi zina zambiri, ndipo zisindikitseni muchinenero chanuchanu mu timabuku tathu ta Botanix! Lumikizanani nafe kuti mumve zambiri.

Category: Zonse Bowa Malangizo a kalimidwe ka mbewu Mapalmu Tizilombo towononga mbewu Udzu Zomera za chilendo Zomera za m’madzi